Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Timoteo 4:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pa codzikanira canga coyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; cimeneco cisawerengedwe cowatsutsa.

17. Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine cilalikiro cimveke konse konse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.

18. Ambuye adzandilanditsa ku nchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wace wa Kumwamba; kwa iye ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.

19. Lankhula Priska ndi Akula, ndi banja la Onesiforo.

20. Erasto anakhalira m'Korinto; koma Trofimo ndamsiya wodwala ku Mileto.

21. 1 Tayesetsa kudza isanadze nyengo yacisanu. Akulankhula iwe Eubulo, ndi Pude, ndi Lino, ndi Klaudiya, ndi abale onse.

22. 2 Ambuye akhale ndi mzimu wako. Cisomo cikhale nanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Timoteo 4