Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Timoteo 4:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Kristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ace ndi ufumu wace;

2. lalikira mau; cita nao pa nthawi yace, popanda nthawi yace; tsutsa, dzudzula, cenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi ciphunzitso.

3. Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:

4. ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe.

5. Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, cita nchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.

6. Pakuti ndirimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.

7. Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga cikhulupiriro:

8. cotsalira wandiikira ine korona wa cilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ace.

9. Tayesetsa kudza kwa ine msanga:

10. pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalimatiya.

Werengani mutu wathunthu 2 Timoteo 4