7. ophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufikira ku cizindikiritso ca coonadi.
8. Ndipo monga momwe Yane ndi Yambre anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana naco coonadi; ndiwo anthu obvunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pacikhulupiriro.
9. Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.
10. Koma iwe watsatatsata ciphunzitso canga, mayendedwe, citsimikizo mtima, cikhulupiriro, kuleza mtima, cikondi, cipiriro,
11. mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandicitira m'Antiokeya, m'Ikoniya, m'Lustro, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.
12. Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.