Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Timoteo 2:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Uwakumbutse izi, ndi kuwacitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asacite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.

15. Ucite cangu kudzionetsera kwa Mulungu wobvomerezeka, wanchito wopanda cifukwa ca kucita manyazi, wolunjika nao bwino mau a coonadi.

16. Koma pewa nkhani zopanda pace; pakuti adzapitirira kutsata cisapembedzo,

17. ndipo mau ao adzanyeka cironda; a iwo ali Humenayo ndi Fileto;

18. ndiwo amene adasokera kunena za coonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwacitika kale, napasula cikhulupiriro ca ena.

19. Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi cukhala naco cizindikilo ici, Ambuye azindikira iwo amene ali ace; ndipo, Adzipatule kwa cosalungama yense wakuehula dzina la Ambuye.

20. Koma m'nyumba yaikuru simuli zotengera za golidi ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.

21. Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala cotengera ca kuulemu, copatulidwa, coyenera kucita naco Mbuye, cokonzera nchito yonse yabwino.

22. Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate cilungamo, cikhulupiriro, cikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.

23. Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu.

24. Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kucita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,

25. 1 wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; 2 ngati kapena Mulungu awapatse iwo citembenuziro, kukazindikira coonadi,

26. ndipo 3 akadzipulumutse ku msampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, ku cifuniro cace.

Werengani mutu wathunthu 2 Timoteo 2