Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Timoteo 2:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'cisomo ca m'Kristu Yesu.

2. Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.

3. Umve zowawa pamodzi nane monga msilikari wabwino wa Kristu Yesu.

4. Msilikari sakodwa nazo nchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikari.

5. Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani a masewero, sambveka korona ngati sanayesana monga adapangana.

6. Wam'munda wogwiritsitsa nchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozoo

7. Lingirira cimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa cidziwitso m'zonse.

8. Kumbukila Yesu Kristu, wouka kwa akufa, wocokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;

9. m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wocita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.

10. Mwa ici ndipirira zonse, cifukwa ca osankhika, kuti iwonso akapeze cipulumutsoeo ca mwa Kristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.

11. Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi iye, tidzakhalanso moyo ndi iye:

Werengani mutu wathunthu 2 Timoteo 2