Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Petro 3:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Popezaizi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'cipembedzo,

12. akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwace kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha mota idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukuru.

13. Koma monga mwa lonjezano lace tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi ziko latsopano m'menemo mukhalitsa cilungamo.

14. Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, citani cangu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda cirema.

15. Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu cipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa cwa iye, anakulemberani;

16. monganso m'akalata ace onse pokanba momwemo za izi; m'menemo nuli zina zobvuta kuzizindikira, zinene anthu osaphunzira ndi osachazikika apotoza, monganso atero lao malembo ena, ndi kudziononga lao eni.

17. Inu, tsono, okondedwa, oozizindikiratu izi, cenjerani, kuti ootengedwa ndi kulakwa kwa iwo osayeruzika, mungagwe kusiya cichazikiko canu.

18. Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi Yesu vistu; kwa iye kukhale uleme'ero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.

Werengani mutu wathunthu 2 Petro 3