Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Petro 2:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pace, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo;

19. ndi kuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo okha ali aka polo a cibvundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wace.

20. Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa cizindikiritsoca, Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zorsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo,

21. Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya cilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.

22. Cidawayenera iwo ca nthanthi yoona, Garu wabwerera ku masanzi ace, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m'thope.

Werengani mutu wathunthu 2 Petro 2