Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Petro 2:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha citayiko cakudza msanga.

2. Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; cifukwa ca iwo njira ya coonadi idzanenedwa zamwano.

3. Ndipo m'cisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene ciweruzo cao sicinacedwa ndi kale lomwe, ndipo citayiko cao siciodzera.

4. Pakuti ngati Mulungu sanalekerera angelo adacimwawo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzidwe;

5. ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa cilungamo, ndi anzace asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza cigumula;

6. ndipo pakuisandutsa makara midzi ya Sodoma ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika citsanzo ca kwa iwo akakhala osapembedza;

7. ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja

8. (Pakuti wolungamayo pokhala pakati pao, ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wace wolungama tsiku ndi tsiku ndi nchito zao zosayeruzika).

9. Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;

10. kama makamaka iwo akutsata zathupi, m'cilakolako ca zodetsa, napeputsa cilamuliro; osaopa kanthu, otsata cifuniro ca iwo eni, santhunthumira kucitira mwano akulu;

11. popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakucita mwano.

Werengani mutu wathunthu 2 Petro 2