Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Petro 1:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo ndiciyesa cokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;

14. podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Kristu anandilangiza.

15. Koma ndidzacitanso cangu kosalekeza kuti nditacoka ine, mudzakhoza kukumbukila izi,

16. Pakuti sitinatsata miyambi yacabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m'maso ukulu wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Petro 1