Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Atesalonika 2:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo cifukwa cace Mulungu atumiza kwa iwo macitidwe a kusoceretsa, kuti akhulupirire bodza;

12. kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira coonadi, komatu anakondwera ndi cosalungama.

13. Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi, mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi;

14. kumene aoaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Kristu.

15. Cifukwa cace tsono, abale, cirimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu.

16. Ndipo Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa elsangalatso cosatha ndi ciyembekezo cokoma mwa cisomo,

17. asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu nchito yonse ndi mau onse abwino.

Werengani mutu wathunthu 2 Atesalonika 2