Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi, mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi;