Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 9:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. kuti kapena akandiperekeze a ku Makedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingacititsidwe manyazi m'kulimbika kumene.

5. Cifukwa cace ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti cikhale cokonzeka comweci, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.

6. Koma nditi ici, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.

7. Yense acite monga anatsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

8. Ndipo Mulungu akhoza kucurukitsira cisomo conse kwa inu; kuti inu, pokhala naco cikwaniro conse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukacurukire ku nchito yonse yabwino;

9. monga kwalembedwa;Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka;Cilungamo cace cikhala ku nthawi yonse.

10. Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale cakudya, adzapatsa ndi kucurukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za cilungamo canu;

11. polemeretsedwa inu m'zonse ku kuolowa manja konse, kumene kucita mwa ife ciyamiko ca kwa Mulungu,

12. Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma ucurukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;

13. popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonia kwa cibvomerezo canu ku Uthenga Wabwino wa Kristu, ndi kwa kuolowa manja kwa cigawano canu kwa iwo ndi kwa onse;

14. ndipo iwo, ndi pempherero lao la kwa inu, akhumbitsa inu, cifukwa ca cisomo coposa ca Mulungu pa inu,

15. Ayamikike Mulungu cifukwa ca mphatso yace yace yosatheka kuneneka.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 9