Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 9:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. pakuti ndidziwa cibvomerezo canu cimene ndidzitamandira naco cifukwa ca inu ndi Amakedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu citapita caka; ndi cangu canu cinautsa ocurukawo.

3. Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pace m'menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;

4. kuti kapena akandiperekeze a ku Makedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingacititsidwe manyazi m'kulimbika kumene.

5. Cifukwa cace ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti cikhale cokonzeka comweci, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.

6. Koma nditi ici, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.

7. Yense acite monga anatsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

8. Ndipo Mulungu akhoza kucurukitsira cisomo conse kwa inu; kuti inu, pokhala naco cikwaniro conse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukacurukire ku nchito yonse yabwino;

9. monga kwalembedwa;Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka;Cilungamo cace cikhala ku nthawi yonse.

10. Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale cakudya, adzapatsa ndi kucurukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za cilungamo canu;

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 9