Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 9:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;

2. pakuti ndidziwa cibvomerezo canu cimene ndidzitamandira naco cifukwa ca inu ndi Amakedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu citapita caka; ndi cangu canu cinautsa ocurukawo.

3. Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pace m'menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;

4. kuti kapena akandiperekeze a ku Makedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingacititsidwe manyazi m'kulimbika kumene.

5. Cifukwa cace ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti cikhale cokonzeka comweci, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 9