Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 7:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti cisoni ca kwa Mulungu citembenuzira mtima kueipulumutso, cosamvetsanso cisoni; koma cisonicadziko lapansi cicita imfa.

11. Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.

12. Cifukwa cace ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinacita cifukwa ca iye amene anacita coipa, kapena cifukwa ca iye amene anacitidwa coipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.

13. Cifukwa ca icitatonthozedwa; ndipo m'citonthozo cathu tinakondwera koposa ndithu pa cimwemwe ca Tito, kuti mzimu wace unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.

14. Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye cifukwa ca inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'coonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala coonadi.

15. Ndipo cikondi ceni ceni care cicurukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.

16. Ndikondwera kuti m'zonse ndilimbika mtima za inu.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 7