Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 3:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakutinso cimene cinacitidwa ca ulemerero sicinacitidwa ca ulemerero m'menemo, cifukwa ca ulemerero woposawo.

11. Pakuti ngati cimene cirikucotsedwa cinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri cotsalaco ciri m'ulemerero.

12. Pokhala naco tsono ciyembekezo cotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukuru,

13. ndipo si monga Mose, amene anaika cophimba pa nkhope yace, kuti ana a lsrayeli asayang'anitse pa cimariziro ca cimene cinalikucotsedwa;

14. koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa lcuwerenga kwa pangano lakale cophimba comweci cikhalabe cosabvundukuka, cimene cirikucotsedwa mwa Kristu.

15. Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, cophimba cigona pamtima pao.

16. Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, cophimbaco cieotsedwa.

17. Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 3