Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 3:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kodi tirikuyambanso kudzibvomereza tokha? kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otibvomerezetsa kwa inu, kapena ocokera kwa inu?

2. Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;

3. popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosatim'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.

4. Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Kristu:

5. si kuti tiri okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mocokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kucokera kwa Mulungu;

6. amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la cilembo, koma la mzimu; pakuti cilembo cipha, koma mzimu ucititsa moyo.

7. Komangati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolocedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sanathe kuyang'anitsa pankhope yace ya Mose, cifukwa ca ulemerero wa nkhope yace, umene unalikucotsedwa:

8. koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala m'ulemerero?

9. Pakuti ngati utumiki wa citsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa cilungamo ucurukira muulemerero kwambiri.

10. Pakutinso cimene cinacitidwa ca ulemerero sicinacitidwa ca ulemerero m'menemo, cifukwa ca ulemerero woposawo.

11. Pakuti ngati cimene cirikucotsedwa cinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri cotsalaco ciri m'ulemerero.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 3