Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 13:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nthawi yacitatu iyi ndirinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.

2. Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kaciwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adacimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;

3. popeza mufuna citsimikizo ca Kristu wakulankhula mwa ine; amene safoka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;

4. pakuti anapacikidwa m'ufoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tiri ofok a mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.

5. Dziyeseni nokha, ngati muli m'cikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Kristu ali mwa inu? mukapanda kukhala osatsimikizidwa.

6. Koma ndiyembekeza kuti mudzazindikira kuti sitiri osatsimikizidwa.

7. Ndipo tipemphera Mulungu kuti musacite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke obvomerezeka, koma kuti inu mukacite cabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.

8. Pakuti sitikhoza kanthu pokana coonadi, koma pobvomereza coonadi.

9. Pakuti tikondwera, pamene ife tffoka ndi inu muli amphamvu; icinso tipempherera, ndicoungwiro wanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 13