Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 12:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Za ici ndinapemphera Ambuye katatu kuti cicoke rkwafne.

9. Ndipo ananena kwa ine, Cisomo canga cikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufoko. Cifukwa cace makamaka ndidzadzitamandira rriokondweratu m'maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine.

10. Cifukwa cace ndisangalala m'tnaufoko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, cifukwa ca Kristu; pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndiri wamphamvu.

11. Ndakhala wopanda nzeru, mwandtcititsa kutero; pakuti inu nunayenera kundibvomereza; pacuti sindiperewera ndi atumwiopoiatu m'kanthu konse, ndingakhale adiri cabe.

12. Zizindikilotu za ntumwi zinacitika pakati pa inu, ri'cipiriro conse, ndi zizindikilo, ndi cozizwa, ndi zamphamvu.

13. Pakuti kuli ciani cimene munacepetsedwa naco ndi Mipingo yotsala yina, agati, si ici kuti ine ndekha sindirasaukitsa inu? Ndikhululukireni oipa ici.

14. Taonani, nthawi yaitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa nu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; cakuti ana sayenera kuunjikira atate adi amai, koma atate ndi amai kumjikira ana.

15. Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse cifucwa ca miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kocuruka koposa, kodi ndikondedwa kocepa?

16. Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wocenjera ine, ndinakugwirani ndi cinyengo.

17. Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakucenjererani naye kodi? Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 12