Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 1:12-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa cikumbu mtima cathu, kuti m'ciyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'cisomo ca Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.

13. Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga, kapenanso mubvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti mudzabvomereza kufikira cimariziro;

14. monganso munatibvomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.

15. Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhalenaco cisomo caciwiri;

16. ndipo popyola kwanu kupita ku Makedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Makedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.

17. Pamenepo, pakufuna cimene, kodi ndinacitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?

18. Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhala eya ndi iai.

19. Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silvano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa iye.

20. Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa iye eya; cifukwa cacenso ali mwa iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

21. Koma iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Kristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;

22. amenenso anatisindikiza cizindikilo, natipatsa cikole ca Mzimu mu mitima yathu.

23. Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kud kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.

24. Si kuti ticita ufumu pa cikhulupiriro canu, koma tikhala othandizana naco cimwemwe canu; pakuti ndi cikhulupiriro muimadi.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 1