Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 1:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya lonse:

2. Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.

3. Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa citonthozo conse,

4. woo titonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iri yonse, mwa citonthozo cimene titonthozedwa naco tokha ndi Mulungu.

5. Pakuti monga masautso a Kristu aticurukira ife, coteronso citonthozo cathu cicuruka mwa Kristu,

6. Koma ngati tisautsidwa, kuli cifukwa ca citonthozo ndi cipulumutso canu; ngati titonthozedwa, kuli kwa citonthozo canu cimene cicititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 1