Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 5:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; cifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anacita umboni za Mwana wace.

10. Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; ye wosakhulupirira Mulungu ananuyesa iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana wace.

11. Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wace.

12. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.

13. Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.

14. Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera;

15. ndipo ngati tidziwa kuti atimvera ciri conse ticipempha, tidziwa kuti tiri nazo izi tazipempha kwa iye.

16. Wina akaona mbale wace alikucimwa cimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo iye adzampatsira moyo wa iwo akucita macimo osati a kuimfa. Pali cimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.

17. Cosalungama ciri conse ciri ucimo; ndipo pali cimo losati la kuimfa.

18. Tidziwa kuti yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacimwa, koma iye wobadwa kucokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.

19. Tidziwa kuti tiri ife ocokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.

20. Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife cidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tiri mwa Woonayo, mwa Mwana wace Yesu Kristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.

21. Tiana, 1 dzisungireni nokha kupewa mafano.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 5