Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 5:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Kristu wabadwa kucokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wocokera mwa iye.

2. Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kucita malamulo ace.

3. Pakuti ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ace: ndipo malamulo ace sali olemetsa.

4. Pakuti ciri conse cabadwa mwa Mulungu cililaka dziko lapansi; ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiriro cathu.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 5