1. Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Kristu wabadwa kucokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wocokera mwa iye.
2. Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kucita malamulo ace.
3. Pakuti ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ace: ndipo malamulo ace sali olemetsa.