Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 4:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Inu ndinu ocokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti iye wakukhah mwa inu aposa iye wakukhala m'dzi ko lapansi. Iwo ndiwo ocoken m'dziko lapansi;

5. mwa ici alankhula monga ocokera m'dziko lapansi, ndipo dziko tapansi liwamve ra.

6. Ife ndife ocokera mwa Mu lungu; iye amene azindikira Mu lungu atimvera; iye wosacoken mwa Mulungu satimvera ife. Mo mwemo tizindikira mzimu wa coonadi, ndi mzimu wa cisokeretso.

7. Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu,

8. iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.

9. Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.

10. Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu.

11. Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 4