Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 4:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.

16. Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.

17. M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.

18. Mulibe mantha m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.

19. Tikonda ife, cifukwa anayamba iye kutikonda.

20. Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wace, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale ware amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.

21. Ndipo lamulo ili tiri nalo locokera kwa iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wace.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 4