Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 3:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kucita ndi m'coonadi.

19. Umo tidzazindikira kuti tiri ocokera m'coonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pace,

20. 1 m'mene monse mtima wathu utitsutsa; cifukwa Mulungu ali wamkuru woposa mitima yathu, nazindikira zonse.

21. Okondedwa, 2 mtima wathu ukapanda kuritsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu;

22. ndipo 3 cimene ciri conse tipempha, tilandira kwa iye, cifukwa tisunga malamulo ace, ndipo ticita zomkondweretsa pamaso pace.

23. Ndipo 4 Lamulo lace ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wace Yesu Kristu, ndi 5 kukondana wina ndi mnzace, monga anatilamulira.

24. Ndipo 6 munthu amene asunga malamulo ace akhala mwa iye, ndi iye mwa munthuyo. Ndipo 7 m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kucokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 3