Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 3:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma iye amene ali naco coma ca dziko lapansi, naona mbale wace ali wosowa ndi kutsekereza cifundo cace pommana iye, nanga cikondi ca Mulungu cikhala mwa iye bwanji?

18. Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kucita ndi m'coonadi.

19. Umo tidzazindikira kuti tiri ocokera m'coonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pace,

20. 1 m'mene monse mtima wathu utitsutsa; cifukwa Mulungu ali wamkuru woposa mitima yathu, nazindikira zonse.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 3