Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 2:26-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.

27. Ndipo inu, 8 kudzoza kumene munalandira kucokera kwa iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma 9 monga kudzoza kwace kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa iye.

28. Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa iye; kuti 10 akaonekere iye tikakhale nako kulimbika mtima, osacita manyazi kwa iye pa kudza kwace.

29. Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti 11 ali yensenso wakucita cilungamo abadwa kucokera mwa iye.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 2