Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 2:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Sindinakulemberam cifukwa simudziwa coonadi, koma cifukwa muddziwa, ndi cifukwa kulibe bodza locokera kwa coonadi.

22. 4 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Kristu? iye ndiye wokana Kristu, amene akana Atate ndi Mwana.

23. 5 Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wobvomereza Mwana ali ndi Atatenso.

24. Koma inu, cimene munacimva kuyambira paciyambi cikhale mwa Inu, 6 Ngari cikhala mwa inu cimene mudacimva kuyambira paciyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.

25. Ndipo 7 ili ndi lonjezano iye anatiloniezera ife, ndiwo moyo wosatha.

26. Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.

27. Ndipo inu, 8 kudzoza kumene munalandira kucokera kwa iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma 9 monga kudzoza kwace kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa iye.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 2