Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 2:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musacimwe. Ndipo akacimwa wina, Nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama;

2. ndipo iye ndiye ciombolo ca macimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.

3. Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira iye, ngati tisunga malamulo ace.

4. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa iye, koma wosasunga malamulo ace, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe coonadi;

5. koma iye amene akasunga mau ace, mwa iyeyu zedi cikondi ca Mulungu cathedwa. M'menemo tizindikira kuti tiri mwa iye;

6. iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wace kuyenda monga anayenda Iyeyo.

7. Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa ciyambi; Lamulo Iakaielo ndilo mau amene mudawamva.

8. Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndico cimene ciri coona mwa iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala,

9. iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wace, ali mumdima kufikira tsopane lino.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 2