Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 6:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. limene adzalionetsa m'nyengo za iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye;

16. amene iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona; kwa iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.

17. Lamulira iwo acuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere cuma cosadziwika kukhala kwace, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kocurukira, kuti tikondwere nazo;

18. kuti acite zabwino, naeuruke ndi nchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;

19. nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weni weniwo.

20. Timoteo iwe, dikira cokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pace ndi zotsutsana za ici cichedwa cizindikiritso konama;

21. cimene ena pocibvomereza 1 adalakwa ndi kutaya cikhulupiriro. Cisomo cikhale nanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 6