Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 3:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda cifukwa.

11. Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.

12. Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.

13. Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukuru m'cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.

14. Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posacedwa, koma ngati ndicedwa,

15. kuti udziwe kuyenedwa kwace pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Eklesia wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mcirikizo wa coonadi.

16. Ndipo pobvomerezeka, cinsinsi ca kucitira Mulungu ulemu ncacikuru: iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 3