Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 2:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu), mwa nchito zabwino.

11. Mkazi aphunzire akhale wacete m'kumvera konse.

12. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.

13. Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;

14. ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;

15. koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'cikhulupiriro ndi cikondi ndi ciyeretso pamodzi ndi cidziletso.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 2