Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Pempherero la kwa anthu onset

1. Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti acitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, cifukwa ca anthu onse;

2. cifukwa ca mafumu ndi onse akucita ulamuliro kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima, ndi acete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.

3. Pakuti ici ncokoma ndi colandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;

4. amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi.

5. Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu,

6. amene anadzipereka yekha ciombolom'malo mwa onse; umboni m'nyengo zace;

7. umene anandiika ine mlaliki wace ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'cikhulupiriro ndi coonadi.

8. Cifukwa cace ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.

Zoyenera akazi

9. Momwemonso, akazi adzibveke okha ndi cobvala coyenera, ndi manyazi, ndi cidziletso; osati ndi tsitsi lace loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena maraya a mtengo wace wapatali;

10. komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu), mwa nchito zabwino.

11. Mkazi aphunzire akhale wacete m'kumvera konse.

12. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.

13. Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;

14. ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;

15. koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'cikhulupiriro ndi cikondi ndi ciyeretso pamodzi ndi cidziletso.