Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 5:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. ameneyo mumkanize okhazikika m'cikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zirimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.

10. Ndipo Mulungu wa cisomo conse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wace wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda cirema mwini wace, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

11. Kwa iye kukhale mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.

12. Mwa Silvano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwacidule, ndi kudandaulira, ndi kucita umboni, kuti cisomo coona ca Mulungu ndi ici; m'cimeneci muimemo.

13. Iye wa ku Babulo wosankhidwa pamodzi nanu akulankhulani; ateronso Marko mwana wanga.

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 5