Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 4:2-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma cifuniro ca Mulungu.

3. Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kucita cifuno ca amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

4. m'menemo ayesa ncacilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa citayiko, nakucitirani mwano;

5. amenewo adzamwerengera iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.

6. Pakuti cifukwa ca ici walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m'thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.

7. Koma citsiriziro ca zinthu zonse ciri pafupi; cifukwa cace khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;

8. koposa zonse mukhale naco cikondano ceni ceni mwa inu nokha; pakuti cikondano cikwiriritsa unyinji wa macimo;

9. mucerezane wina ndi mnzace, osadandaula:

10. monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a cisomo ca mitundu mitundu ca Mulungu;

11. akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, acite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.

12. Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale cakukuyesani, ngati cinthu cacilendo cacitika nanu:

13. koma popeza mulawana ndi Kristu zowawa zace, kondwerani; kutinso pa bvumbulutso la ulemerero wace mukakondwere kwakukurukuru.

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 4