Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 3:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.

5. Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;

6. monga Sara anamvera Abrahamu, namucha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ace ngati mucita bwino, osaopa coopsa ciri conse.

7. Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa cidziwitso, ndi kucitira mkazi ulemu, monga cotengera cocepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa cisomo ca moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.

8. Cotsalira, khalani nonse a mdma umodzi, ocitirana cifundo, okondana ndi abale, acisoni, odzicepetsa:

9. osabwezera coipa ndi coipa, kapena cipongwe ndi cipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ici mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.

10. Pakuti,iye wofuna kukonda moyo,Ndi kuona masiku abwino,Aletse lilime lace lisanene coipa,Ndi milomo yace isalankhule cinyengo;

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 3