Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 2:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kun mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu,

6. Cifukwa kwalembedwa m'lembo,Taona, ndiika m'Ziyoni mwala wotsiriza wa pangondya, wosankhika, wa mtengo wace;Ndipo wokhulupirira iye sadzanyazitsidwa.

7. Kwa inu tsono akukhulupira, ali wa mtengo wace; koma kwa iwo osakhulupira,Mwala umene omangawo anaukana,Womwewo unayesedwa mutu wa pangondya;

8. ndipo,Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa;kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.

9. Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa;

10. inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira cifundo, koma tsopano mwalandira cifundo.

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 2