Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PETRO, mtumwi wa Yesu Kristu, kwa osankhidwa akukhala: alendo a cibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,

2. monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.

3. Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa cifundo cace cacikuru, anatibalanso ku ciyembekezo ca moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu;

4. kuti tilandire colowa cosabvunda ndi cosadetsa ndi cosafota, cosungikira m'Mwamba inu,

5. amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa cikhulupiriro, kufikira cipulumutso cokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza.

6. M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukacitidwe cisoni ndi mayesero a mitundu mitundu,

7. kuti mayesedwe a cikhulupiriro canu, ndiwo a mtengo wace woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ocitira ciyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu, Kristu;

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 1