Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 5:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma ife popeza tiri a usana tisaledzere, titabvala capacifuwa ca cikhulupiriro ndi cikondi; ndi cisoti ciri ciyembekezo ca cipulumutso.

9. Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire cipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu,

10. amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.

11. Mwa ici cenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzace, monganso mumacita,

12. Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa nchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyatnbirirani inu;

13. ndipo muwacitire ulemu woposatu mwa cikondi, cifukwa ca nchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.

14. Koma tidandaulira inu abale, yambirirani ampwayi, limbikitsani amantha mtima? cirikizani ofok a, mukhale oleza mtima pa onse.

15. Penyani kuti wina asabwezere coipa womcitira coipa; komatu nthawi zonse mutsatire cokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.

16. Kondwerani nthawi zonse;

17. Pempherani kosaleka;

18. M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.

19. Musazime Mzimuyo;

20. Musanyoze maaenero;

21. Yesani zonse; sungani cokomaco,

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 5