Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 5:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitiri a usiku, kapena a mdima;

6. cifukwa cace tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere,

7. Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.

8. Koma ife popeza tiri a usana tisaledzere, titabvala capacifuwa ca cikhulupiriro ndi cikondi; ndi cisoti ciri ciyembekezo ca cipulumutso.

9. Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire cipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu,

10. amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.

11. Mwa ici cenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzace, monganso mumacita,

12. Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa nchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyatnbirirani inu;

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 5