Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 2:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sanakhala opanda pace;

2. koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anaticitira cipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.

3. Pakuti kudandaulira kwathu sikucokera kukusocera, kapena kucidetso, kapena m'dnyengo;

4. komatu monga Mulungu anatibvomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.

5. Pakuti sitinayenda nao mau osyasyalika nthawi iri yonse, monga mudziwa, kapena kupsiniira msiriro, mboni ndi Mulungu;

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 2