Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 9:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za kacisi amadya za m'Kacisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

14. Comweconso Ambuyeanalamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

15. Koma ine sindinacita nako kanthu kaizi; ndipo sindilemba izi kuti cikakhale cotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwacabe kudzitamanda kwanga.

16. Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndiribe kanthu kakudzitamandira; pakuti condikakamiza ndigwidwa naco; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira U thenga Wabwino.

17. Pakuti ngati ndicita ici cibvomerere, mphotho ndiri nayo; koma ngati si cibvomerere; anandikhulupirira m'udindo.

18. Mphotho yanga nciani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.

19. Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ocuruka.

20. Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;

21. kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo twa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 9