Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 9:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kodi sindine mfulu? Kodi slndine mtumwi? Kodi sindinaona Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu nchito yanga mwa Ambuye?

2. Ngati sindiri mtumwi kwa ena, komatu ndiri kwa inu; pakuti cizindikilo ca utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.

3. Codzikanira canga kwa iwoamene andifunsa ine ndi ici:

4. Kodi tiribe ulamuliro wa kudya ndi kumwa?

5. Kodi tiribe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?

6. Kapena kodi ife tokha, Bamaba ndi ine, tiribe ulamuliro wakusagwira nchito?

7. Msilikari ndani acita nkhondo, nthawi iriyonse, nadzifunira zace yekha? Aoka mipesa ndani, osadya cipatso cace? Kapena aweta gulu ndani, osadyamkaka wace wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

8. Kapena cilamulo sieinenanso zomwezo?

9. Pakuti m'cilamulo ca Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe?

10. Kapena acinena ici konse konse cifukwa ca ife? Pakuti, cifukwa ca ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa ciyembekezo, ndi wopunthayo acita mwa ciyembekezo ca kugawana nao.

11. Ngati takufeserani inu zauzimu, kodi ncacikuru ngati ife tituta za thupi lanu?

12. Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinacita nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingacite cocedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Kristu,

13. Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za kacisi amadya za m'Kacisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

14. Comweconso Ambuyeanalamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

15. Koma ine sindinacita nako kanthu kaizi; ndipo sindilemba izi kuti cikakhale cotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwacabe kudzitamanda kwanga.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 9