Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 8:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tid naco cidziwitso tonse. Cidziwitso citukumula, koma cikondicimangirira.

2. Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.

3. Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi iye.

4. Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano siliri kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.

5. Pakuti ngakhalenso iriko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iriko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;

6. koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zicokera kwa iye, ndi ire kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife mwa iye.

7. Komatu cidziwitso siciri mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo cikumbu mtima cao, popeza ncofoka, cidetsedwa.

8. Koma cakudya sicitibvomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tiribe kupindulako,

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 8