Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Musakanizana, koma ndi kubvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, cifukwa ca kusadziletsa kwanu.

6. Koma ici ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira.

7. Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndiri ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yace ya iye yekha kwa Mulungu, wina cakuti, wina cakuti.

8. Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.

9. Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

10. Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,

11. komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.

12. Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkaziwosakhulupira, ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7