Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:37-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwace, wopanda cikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa cifuniro ca iye yekha, natsimikiza ici mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wace wamkazi, adzacita bwino.

38. Cotero iye amene akwatitsa mwana wace wamkazi acita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa acita koposa.

39. Mkazi amangika pokhala mwamuna wace ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.

40. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndiganiza kuti inenso ndiri naye Mzimu wa Mulungu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7