Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:2-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Koma cifukwa ca madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

3. Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ace; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.

4. Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lace la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi laiye yekha, koma mkazi ndiye.

5. Musakanizana, koma ndi kubvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, cifukwa ca kusadziletsa kwanu.

6. Koma ici ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira.

7. Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndiri ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yace ya iye yekha kwa Mulungu, wina cakuti, wina cakuti.

8. Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.

9. Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

10. Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,

11. komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.

12. Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkaziwosakhulupira, ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.

13. Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupira, nabvomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo.

14. Pakuti mwamuna wosakhulupirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.

15. Koma ngati wosakhulupirayo acoka, acoke. M'mirandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo, Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.

16. Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7