Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika m'Mipingo yonse.

18. Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe.

19. Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.

20. Yense akhale m'maitanidwe m'mene anaitanidwamo.

21. Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, cita nako ndiko.

22. Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Kristu.

23. Munagulidwa ndi mtengo wace; musakhale akapolo a anthu.

24. Yense, m'mene anaitanidwamo, abate, akhale momwemo ndi Mulungu.

25. Koma kunena za anamwali, ndiribe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani coyesa ine, monga wolandira cifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7